Ezra 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti ine mfumu pamodzi ndi aphungu anga asanu ndi aŵiri tikukutuma kuti ukafunsitse za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu, kuti ukaone m'mene anthu akutsatira malamulo amene Mulungu wako adaŵapereka kwa iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza utumidwa wochokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ake asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako lili m'dzanja lako,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine mfumu pamodzi ndi alangizi anga asanu ndi awiri tikukutumani kuti mukafufuze za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu kuti mukaone mmene anthu akutsatira malamulo a Mulungu wanu, amene anawapereka kwa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza utumidwa wocokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ace asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako liri m'dzanja lako,