Ezra 7:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utengenso siliva ndi golide yense amene mumpeze m'dziko lonse la Babiloni, ndiponso zopereka zimene anthu ndi ansembe adzapereka mwaufulu, mosakakamiza, kuperekera Nyumba ya Mulungu wao ya ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mutengenso siliva yense ndi golide amene mungamupeze mʼdziko lonse la Babuloni, ngakhalenso zinthu zimene anthu pamodzi ndi ansembe adzapereka mwaufulu kuperekera ku Nyumba ya Mulungu wawo ya ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamodzi ndi siliva ndi golidi ziri zonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babulo, pamodzi ndi copereka caufulu ca anthu, ndi ca ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao iri ku Yerusalemu;