Ezra 7:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndi ndalama zimenezi, mudzagule mwachangu ng'ombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zake zaufa ndiponso nsembe zake zazakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa la ku Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
m'mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng'ombe, nkhosa zamphongo, anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka pa guwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi ndalama zimenezi mudzaonetsetse kuti mwagula ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa aamuna pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa lansembe la Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
m'mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng'ombe, nkhosa zamphongo, ana a nkhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka pa guwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu.