Ezra 7:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono ine, mfumu Arita-kisereksesi, ndikulamula onse osunga chuma m'dera la Patsidya pa Yufurate, kuti zonse zimene wansembe Ezara, wophunzira wa malamulo a Mulungu Wakumwamba, adzapemphe kwa inu, zichitike mwachangu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano Ine, mfumu Aritasasita, ndikulamula asungichuma onse a dera la Patsidya pa Yufurate kuti, chilichonse chimene wansembe Ezara, mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba adzapempha kwa inu, mupatseni mwa msanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ine Aritasasta, mfumu ine, ndilamulira osunga cuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti ciri conse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, cicitike mofulumira;