Ezra 7:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikukudziŵitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kumkhometsa msonkho uliwonse wansembe aliyense, Mlevi aliyense, woimba aliyense, mlonda kapena wantchito aliyense wa ku Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, Anetini, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tikukudziwitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kukhometsa msonkho uliwonse anthu awa: ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda kapena aliyense wogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa ali yense wa ansembe, ndi Alevi, oyimbira, odikira, Anetini, kapena anchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.