Ezra 7:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndiye iwe Ezara, potsata nzeru zimene Mulungu wako adakupatsazi, usankhe oyendetsa zinthu ndi aweruzi oti azilamulira anthu onse okhala m'dera la Patsidya pa Yufurate, anthu ake otsata malamulo a Mulungu wako. Ndipo anthu osadziŵa malamulowo uzidzaŵaphunzitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwe, Ezara, monga mwa nzeru za Mulungu wako zimene uli nazo, usankhe oyendetsa zinthu ndi oweruza kuti azilamulira anthu onse okhala ku dera la Patsidya pa Yufurate, onse amene amadziwa malamulo a Mulungu wako. Ndipo uphunzitse aliyense amene sawadziwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako iri m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza mirandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.