Ezra 7:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense amene sadzamvera malamulo a Mulungu wako kapena malamulo a mfumu, alangidwe kolimba, kapena kuphedwa, kapena kuchotsedwa m'dzikolo, kapena kumlanda katundu wake, kapena kumponya m'ndende.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m'dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m'kaidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo amene sadzamvera lamulo la Mulungu wako ndi lamulo la mfumu alangidwe kolimba kapena aphedwe kapena achotsedwe mʼdzikolo, kapena katundu wake alandidwe, kapena aponyedwe mʼndende.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ali yense wosacita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpitikitsa m'dziko, kapena kumlanda cuma cace, kapena kummanga m'kaidi.