Ezra 7:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye amenenso adaonetsa chikondi chake chosasinthika pa ine kuti mfumu ndi aphungu ake ndi atsogoleri ake amphamvu andikomere mtima. Ndidalimba mtima popeza kuti Chauta Mulungu wanga anali nane, choncho ndidasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Aisraele kuti apite nane pamodzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ameneyonso waonetsa chikondi chake chosasinthika kwa ine pamaso pa mfumu, alangizi ake ndi nduna zake zamphamvu kuti andikomere mtima. Choncho ndinalimba mtima popeza Yehova, Mulungu wanga anali nane, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Israeli kuti apite nane pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nandifikitsira cifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ace, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israyeli anthu omveka akwere nane limodzi.