Ezra 7:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ezarayu anali wophunzira kwambiri wa za Malamulo amene Chauta, Mulungu wa Israele, adaapereka kwa Mose. Popeza kuti Chauta, Mulungu wake, adaamdalitsa Ezarayo, mfumu Arita-kisereksesi ankamupatsa zonse zimene ankapempha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ezara ameneyu anabwera kuchokera ku Babuloni. Iyeyu anali wophunzira kwambiri za malamulo a Mose, amene Yehova Mulungu wa Israeli anapereka. Mfumu inamupatsa chilichonse chimene anapempha pakuti dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ezara amene anakwera kucokera ku Babulo, ndiye mlembi waluntha m'cilamulo ca Mose, cimene Yehova Mulungu wa Israyeli adacipereka; ndipo mfumu inampatsa copempha iye conse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wace.