Ezra 7:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adanyamuka ku Babiloni pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, nafika ku Yerusalemu ndi chithandizo cha Mulungu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku lachimodzi la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayamba ulendo wochoka ku Babuloni pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo ciyambi ca ulendo wokwera kucokera ku Babulo, ndi tsiku lacimodzi la mwezi wacisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wace.