Ezra 8:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidaŵatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ndidaŵauza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkulu, kumalo dzina lake Kasifiya; ndinalonganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ake Anetini, pa malo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ndinawatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ine ndinawawuza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkuru, ku malo dzina lace Kasifiya; ndinalooganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ace Anetini, pa malo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu.