Ezra 8:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha kutikomera mtima Mulungu wathu, Ido adatitumizira munthu wanzeru, mwana wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israele, dzina lake Serebiya, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi achibale ake, anthu 18 pamodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israele; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ake ndi abale ake khumi mphambu asanu ndi atatu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha kutikomera mtima kwa Mulungu wathu, Ido anatitumizira munthu wanzeru, Serabiya, wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israeli, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi abale ake, anthu 18.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israyeli; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ace ndi abale ace khumi mphambu asanu ndi atatu;