Ezra 8:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti itipatse gulu la asilikali, ena oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo, oti atiteteze kwa adani athu pa njira. Tinali titauza mfumuyo kuti, “Mulungu wathu amaŵadalitsa onse okhulupirira Iye, koma amaŵakwiyira amene salabadako za Iye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikali, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yake ndi mkwiyo wake zitsutsana nao onse akumsiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti atipatse asilikali oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo kuti atiteteze kwa adani athu pa ulendo wathuwu popeza tinali titawuza kale mfumu kuti “Yehova amateteza aliyense amene amamudalira, koma amakwiyira onse amene amamukana.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndinacita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikari, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yace ndi mkwiyo wace zitsutsana nao onse akumsiya.