Ezra 8:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono tidachoka ku mtsinje wa Ahava pa tsiku la 12, pa mwezi woyamba, kupita ku Yerusalemu. Mulungu wathu anali nafe ndipo adatipulumutsa kwa adani athu, makamaka kwa anthu otibisalira pa njira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo tinachoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, kunka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku la khumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, tinachoka ku mtsinje wa Ahava kupita ku Yerusalemu. Ndipo Mulungu wathu anali nafe, ndipo anatiteteza kwa adani athu makamaka otibisalira pa njira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo tinacoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi ciwiri la mwezi woyamba, kumka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira.