Ezra 8:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lachinai lake, m'Nyumba ya Mulungu wathu momwemo, adayesa siliva ndi golide ndi ziŵiya zija, nkuzipereka m'manja mwa wansembe Meremoti, mwana wa Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eleazara mwana wa Finehasi, ndiponso Alevi aŵa: Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Biruyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pa tsiku lachinai siliva ndi golide ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uriya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Finehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Binuyi, Alevi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku la chinayi lake, mʼNyumba ya Mulungu wathu, tinayeza siliva ndi golide ndi ziwiya zija nʼkuzipereka mʼmanja mwa Meremoti mwana wa wansembe Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eliezara mwana wa Finehasi ndiponso Alevi awa: Yozabadi mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binuyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pa tsiku lacinai siliva ndi golidi ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uliya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Pinehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadia mwana wa Binui, Alevi;