Ezra 8:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo anthu amene adabwerako ku ukapolo, onse amene adaatengedwa aja, adapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri, kuperekera Aisraele onse, nkhosa zamphongo 96, anaankhosa 77, ndiponso atonde 12, ngati nsembe yopepesera machimo ao. Zonsezo zinali nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Otengedwa ndende, atatuluka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anthu amene anatengedwa ukapolo aja anabwerera, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israeli: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, kuperekera Aisraeli onse, nkhosa zazimuna 96, ana ankhosa 77, ndiponso mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri ngati nsembe yopepesera machimo. Zonsezi zinali nsembe yopsereza zopereka kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Otengedwa ndende, ataturuka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israyeli, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisrayeli onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, ana a nkhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.