Ezra 9:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitachitika zimenezi, atsogoleri ena adadza kwa ine, nati, “Aisraele, ansembe ndi Alevi sadadzipatule kwa anthu a mitundu iyi yoyandikana nafe: Akanani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito ndi Aamori. Anthu athuwo akuchita nawo zonyansa zaozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israele, ndi nsembe, ndi Alevi, sanadzilekanitse ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito, ndi Aamori.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitachitika izi, atsogoleri anabwera kwa ine nati, “Aisraeli, kuphatikizanso ansembe ndi Alevi, sanadzipatule ku makhalidwe onyansa a anthu a mitundu ina amene ayandikana nafe: Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aigupto ndi Aamori.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israyeli, ndi ansembe, ndi Alevi, sanadzilekanitsa ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amoabu, Aaigupto, ndi Aamori.