Ezra 9:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
amene mudatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki anu. Mudaŵauza kuti, ‘Dziko mukuloŵamo kuti mulilandelo ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya anthu a m'maikomo. Adzaza dziko lonselo ndi zoipa zaozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale cholowa chanu ndilo dziko lodetsedwa mwa chidetso cha anthu a m'maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga ina kufikira nsonga inzake ndi uchisi wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amene munawapereka kudzera mwa atumiki anu aneneri. Inu munati, ‘Dziko limene mukulowamolo kuti likhale cholowa chanu, ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya mʼmayikomo. Ndipo adzaza dzikolo ndi zochita zawo zonyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale colowa canu ndilo dziko lodetsedwa mwa cidetso ca anthu a m'maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga yina kufikira nsonga inzace ndi ucisi wao.