Ezra 9:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake musakwatitse ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, ndipo ana ao aakazi asakwatiwe ndi ana anu aamuna. Musakhale nawo mumtendere kapena kugwirizana nawo pa malonda, ngati mufuna kukhala amphamvu ndi kumadya zabwino za m'dzikomo, ndi kusiyira ana anu dziko limeneli kuti likhale choloŵa chao mpaka muyaya.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthwawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu colowa ca ku nthawi yonse.