Ezra 9:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde zonsezi zatigwera kaamba ka ntchito zathu zoipa ndi uchimo wathu waukulu. Komabe Inu Mulungu wathu, mwangotilanga pang'ono, kuyerekeza ndi kukula kwa kuchimwa kwathu, ndipo mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha ntchito zathu zoyipa ndi uchimo wathu waukulu, komanso pambuyo poona kuti Inu Mulungu wathu simunangotilanga kokha pangʼono kuyerekeza ndi kuchimwa kwathu komanso mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zitatigwera zonsezi cifukwa ca nchito zathu zoipa ndi kuparamula kwathu kwakukuru; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga moticepsera mphulupulu zathu, ndi ku tipatsa cipulumutso cotere;