Ezra 9:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ife nkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu a mitundu ina, amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzakwiya nafe ndi kutiwononga popanda wina wotsala, kapena wina aliyense wopulumuka?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kodi ife nʼkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu amitundu ina amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzatikwiyira ndi kutiwononga kwathunthu popanda wina wotsala kapena wopulumuka?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatana nayo mitundu ya anthu ocita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka?