Ezra 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, Mulungu wa Israele, ndinu achifundo pakuti ife ndife otsala amene tapulumuka, monga m'mene tiliri lero lino. Taima pano pamaso panu, tikuzindikira kuchimwa kwathu. Choncho palibe ndi mmodzi yemwe amene angaime pamaso panu chifukwa cha zochimwazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m'kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova Mulungu wa Israyeli, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tiri pamaso panu m'kuparamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu cifukwa ca ici.