Ezra 9:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nditamva zimenezi, ndidang'amba zovala zanga ndi mwinjiro wanga chifukwa cha chisoni, ndipo ndidazula tsitsi la kumutu kwanga ndi kumwetsula ndevu zanga, nkukhala pansi ndili wotaya mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba chovala changa, ndi malaya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndevu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba cobvala canga, ndi maraya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndebvu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.