Ezra 9:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakhala pansi choncho kufikira nthaŵi yamadzulo. Tsono anthu onse amene ankaopa mau a Mulungu wa Israele, ataona kusakhulupirika kwa obwerako ku ukapolo aja, adayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nandisonkhanira aliyense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israele, chifukwa cha kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nandisonkhanira ali yense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israyeli, cifukwa ca kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.