Ezra 9:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono itakwana nthaŵi ya nsembe yamadzulo, ndidadzidzimuka mumtima mwanga nkuimirira, zovala zanga zong'ambika zija zikali m'thupi. Ndidagwada nkukweza manja anga kwa Chauta, Mulungu wanga,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, chovala changa ndi malaya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, cobvala canga ndi maraya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;