Ezra 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidati, “Inu Mulungu wanga, manyazi ndi chisoni zikundikanikitsa kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa zoipa zathu zakwera kopambana mitu yathu. Ndithu uchimo wathu wakwera mpaka kukafika kumwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamtu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira m'Mwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kucita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zacuruka pamtu pathu, ndi kuparamula kwathu kwakula kufikira m'Mwamba.