Ezra 9:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira nthaŵi ya makolo athu mpaka pano, takhala tikuchimwa kwambiri. Chifukwa cha machimo athuwo, ifeyo pamodzi ndi mafumu athu ndi ansembe athu, atipereka kwa mafumu a m'maiko achikunja, kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu ndiponso kuti atichititse manyazi kwambiri, monga momwe ziliri masiku anomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chiyambire masiku a makolo athu tapalamula kwakukulu mpaka lero lino; ndi chifukwa cha mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kuchitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chifukwa cha machimo athu, ifeyo, mafumu athu, ndi ansembe athu takhala akutipereka mʼmanja mwa mafumu a mitundu ina ya anthu kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu zathu ndi kutichititsa manyazi monga zilili leromu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ciyambire masiku a makolo athu taparamula kwakukuru mpaka lero lino; ndi cifukwa ca mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kucitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino.