Ezra 9:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano pa kanthaŵi kochepaka, Inu Chauta, Mulungu wathu, mwaonetsa kukoma mtima kwanu. Mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kuloŵa m'malo anu oyera. Mwatilimbitsa mtima ndi kutitsitsimutsa kwa kanthaŵi mu ukapolo wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono m'ukapolo wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma tsopano, pa kanthawi kochepa, Inu Yehova Mulungu wathu mwaonetsa kukoma mtima. Inu mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kutipatsa cholowa mʼmalo anu oyera. Mwatipulumutsa ku ukapolo ndi kutipatsa mpumulo pangʼono mu ukapolo wathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa cisomo, kutisiyira cipulumutso, ndi kutipatsa ciciri m'malo mwace mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono m'ukapolo wathu.