Galatians 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngakhale ife, kapena mngelo wocokera Kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.