Galatians 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti asanafike anthu ena amene Yakobe adaaŵatuma, iye ankadya pamodzi ndi abale osakhala Ayuda. Koma atafika iwowo, iye adayamba kudzipatula, osafuna kudya nawonso, chifukwa choopa anthu amene ankafuna kuti omwe sali Ayuda aumbalidwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti asanafike ena ochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti asanafike anthu otumidwa ndi Yakobo, iye ankadya pamodzi ndi anthu a mitundu ina. Koma atafika, iyeyo anachoka pakati pa anthuwo nakakhala pa yekha chifukwa ankaopa anthu a mʼgulu la mdulidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti asanafike ena ocokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe.