Galatians 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale ena onse ochokera ku Chiyuda nawonso adayamba kuchita chiphamaso, kotero kuti ngakhale Barnabasi yemwe adaatengeka nacho chiphamaso chaocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Bamabanso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.