Galatians 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidaaona kuti iwo sakuyenda molunjika, sakutsata choona cha Uthenga Wabwino. Tsono ndidauza Petro pamaso pa onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda, komabe ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga ungakakamize bwanji anthu a mitundu ina kukhala ngati Ayuda?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nditaona kuti iwo sankachita molingana ndi choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinawuza Petro pamaso pa anthu onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda koma ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga nʼchifukwa chiyani ukukakamiza anthu a mitundu ina kuti akhale ngati Ayuda?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa coonadi ca Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukangamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?