Galatians 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngati ifeyo, poyesetsa kusanduka olungama mwa Khristu, tikupezeka kuti ndifenso ochimwa, kodi pamenepo ndiye kuti Khristu ndi wotumikira uchimo? Mpang'ono pomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Khristu, tipezedwanso tili ochimwa tokha, kodi Khristu ali mtumiki wa uchimo chifukwa chake? Msatero ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono ngati ife, pamene tikufuna kulungamitsidwa mwa Khristu, zikuonekeratu poyera kuti ndifenso ochimwa, kodi zikutanthauza kuti Khristu amalimbikitsa uchimo? Ayi. Nʼkosatheka!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Kristu, tipezedwanso tiri ocimwa tokha, kodi Kristu ali mtumikiwa ucimo cifukwa cace? Msatero ai.