Galatians 2:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi mayo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao: tsopano m'thupi, ndiri nao m'cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.