Galatians 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe, Petro ndi Yohane, amene anthu ankaŵaona kuti ndi mizati mu Mpingo, adazindikira kuti ineyo Mulungu adandipatsadi ntchito imeneyi. Motero adagwirana chanza ndi ine ndiponso ndi Barnabasi, kutsimikiza chiyanjano chathu. Ndipo tidavomerezana kuti ine ndi Barnabasi tipite kwa anthu a mitundu ina, iwowo apite kwa Ayuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo, Petro ndi Yohane, amene ankatengedwa ngati mizati, atazindikira chisomo chimene chinapatsidwa kwa ine, anagwirana chanza ndi ine ndi Barnaba kusonyeza chiyanjano chathu. Iwo anavomereza kuti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa Ayuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pakuzindikira cisomoco cinapatsidwakwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Bamaba dzanja lamanja la ciyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;