Galatians 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene amadalira ntchito za Malamulo ndi otembereredwa. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene satsata zonse zolembedwa m'buku la Malamulo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti onse amene atama nchito za lamulo Iiwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa ali yense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la cilamulo, kuzicita izi.