Galatians 3:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kristu anatiombola ku temberero la cilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa ali yense woo paeikidwa pamtengo;