Galatians 3:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, ndikufotokozereni zimenezi pokupatsani chitsanzo cha zimene zimachitika tsiku ndi tsiku. Anthu aŵiri akapangana natsimikiza chimodzi, palibe munthu angaphwanye panganolo kapena kuwonjezapo mau.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abale, ndinena monga munthu Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesacabe, kapena kuonjezapo.