Galatians 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mulungu adapatsa malonjezo ake kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sakunena kuti, “Ndi kwa mbeu zake” ai, ngati kuti akunena za anthu ambiri. Koma akunena kuti, “Ndi kwa mbeu yake”, popeza kuti akukamba za munthu mmodzi yekha. Ameneyu ndi Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace, Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Kristu.