Galatians 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu akapatsa munthu madalitso chifukwa munthuyo ndi wotsata Malamulo, ndiye kuti madalitsowo sapatsidwanso chifukwa cha lonjezo ai. Koma Mulungu adadalitsa Abrahamu chifukwa adaalonjeza kutero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati kulowa nyumba kucokera kulamulo, sikucokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.