Galatians 3:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga tsono cholinga cha Malamulo chinali chiyani? Mulungu adaonjezapo Malamulo kuti azindikiritse anthu machimo, mpaka mbeu ija ya Abrahamu, imene Mulungu adaaipatsa lonjezo lija, itabwera. Mulungu adapereka Malamulowo kudzera mwa angelo, ndiponso kudzera mwa munthu wochita ntchito ya mkhalapakati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m'dzanja la nkhoswe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga cilamulo tsono? Cinaoniezeka cifukwa ca zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo cinakonzeka ndi angelo m'dzanja la Ilkhoswe.