Galatians 4:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene aja akuchita changu kwambiri pothandiza inu kuti akukopeni, koma changu chaocho sichili chabwino ai. Amangofuna kukupatutsani kuti muzichita changu pakuŵathandiza iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Acita cangu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawacitire iwowa cangu.