Galatians 4:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana amene mai wake anali kapolo uja, adabadwa monga momwe amabadwira ana onse. Koma mwana wina uja, amene mai wake anali mfulu, adabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa Ionjezano, Izo ndizo zophiphiritsa;