Galatians 4:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa ku phiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.