Galatians 4:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Malembo akuti, “Sangalala iwe chumba chosabala ana, imba nthungululu, fuula mokondwera, iwe amene sunamvepo zoŵaŵa za kubala. Ana a mkazi wosiyidwa ndi ochuluka koposa ana a mkazi amene ali naye mwamuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kwalembedwa, Kondwera, chumba iwe wosabala; imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti kwalembedwa kuti, “Sangalala, iwe mayi wosabala, amene sunabalepo mwana; imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kwalembedwa, Kondwera, cumba iwe wosabala; Yimba nthungululu, nupfuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; Pakuti ana ace a iye ali mbeta acuruka koposa ana a iye ali naye mwamuna.