Galatians 4:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga Malembo akuti bwanji? Akuti, “Mpirikitseni kapoloyu pamodzi ndi mwana wake. Mwana wa kapolo asadzakhale konse mloŵachuma pamodzi ndi mwana wa mfulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma lembo linena ciani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wace, pakuti sadzalowa nyumba mwanawa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.