Galatians 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wace alowe m'mitima yathu, wopfuula Abba, Atate.