Galatians 5:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye, kuti simudzakhala ndi maganizo osiyana ndi anga. Koma amene akukusokonezaniyo, ngakhale akhale yani, Mulungu adzamlanga ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakubvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza citsutso cace.