Galatians 5:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kunena za ine, abale, ngati ndikulalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, nanga bwanji ndikuzunzidwabe? Ndikadalalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, sibwenzi ndikuŵakhumudwitsa pakulalika mtanda wa Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, abale, ngati ndilalikiransoindulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo cikhumudwitso ca mtanda cidatha.