Galatians 5:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.